22/07/2024
Bwalo la milandu ku Limbe mu mzinda wa Blantyre lalamula Foster Mathewe Saidi wa zaka 25 kuti akhale kundende zaka 18 kaamba kogwililira msungwana wa zaka 6.
Bwaloli linamvetsedwa kuti mkuluyu pa 21 mwezi watha cha mma 8 koloko usiku adaitana mwanayu yemwe ankadya nsima pa nthawiyo kuti akamugaile ndiwo, koma mwanayo chongolowa m'nyumba mwa mkuluyu, iye adamugwililira.
Koma makolo amwanayu adadabwa kumuona momwe amayendera ndipo atamufunsa iye afotokoza zomwe zidamuchitikira ndipo makolowa adakatula nkhaniyi ku polisi.
Atawonekera ku bwalo la milandu mkuluyu adavomera kulakwa kwake ndipo adapempha bwalo kuti limupatse chilango chofewerapo koma mbali ya boma inati mkuluyu akuyenera chilango chokhwima kuti ena atangerepo phunziro.
Apa ndi pomwe Senior Resident Magistrate Ackia Mwanyongo adati mkuluyu ,yemwe ndi wa m'mudzi mwa Mkawela mfumu yaikulu Inkosi Bvumbwe ku Thyolo, akakhale ku ndende zaka 18 ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga.